Nahum 2:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zishango za ankhondo ao nzofiira, asilikali ao onse avala zovala zamlangali. Atandanda pa mizere yankhondo, magaleta ao akuchezimira ngati malaŵi a moto. Akavalo akungoti jodojodo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zikopa za amphamvu ake zasanduka zofiira, ngwazi zivala mlangali; magaleta anyezimira ndi chitsulo tsiku la kukonzera kwake, ndi mikondo itinthidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zishango za ankhondo ake ndi zofiira; asilikali ake avala zovala zofiirira. Zitsulo za pa magaleta zikunyezimira tsiku la kukonzekera kwake. Akuonetsa mikondo ya mkungudza yonoledwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zikopa za amphamvu ace zasanduka zofiira, ngwazi zibvala mlangali; magareta anyezimira ndi citsulo tsiku la kukonzera kwace, ndi mikondo itinthidwa.