Nahum 3:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe anthu a ku Thebesi adagwidwa, adasanduka akapolo. Ana ao adaŵakankhanthitsa pansi m'miseu yonse ya mumzindamo. Adani adagaŵana anthu otchukawo mwamaere. Akuluakulu onse adaŵamanga ndi maunyolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iye anatengedwa, analowa ndende; ana ake a makanda anaphwanyika polekeza pake pa miseu yake yonse; ndi pa omveka ake anachita maere, ndi akulu ake onse anamangidwa maunyolo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe anthu a ku Tebesi anagwidwa ndipo anapita ku ukapolo. Ana ake anawaphwanyitsa pansi mʼmisewu yonse ya mu mzindamo. Anachita maere ogawana anthu ake otchuka, ndipo anthu ake onse amphamvu anamangidwa ndi maunyolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iye anatengedwa, analowa ndende; ana ace a makanda anaphwanyika polekeza pace pa miseu yace yonse; ndi pa omveka ace anacita maere, ndi akulu ace onse anamangidwa maunyolo.