Nahum 3:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malinga ako onse adzakhala ngati mitengo ya nkhuyu zoyamba kupsa. Akaigwedeza, nkhuyuzo zimagwera m'kamwa mwa wofuna kuzidya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Malinga ako onse adzanga mikuyu ndi nkhuyu zoyamba kupsa; akagwedeza zingokugwa m'kamwa mwa wakudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malo ako onse otetezedwa ali ngati mitengo ya mkuyu yokhala ndi zipatso zoyambirira kucha; pamene agwedeza mitengoyo, nkhuyuzo zimagwera mʼkamwa mwa wofuna kuzidya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Malinga ako onse adzanga mikuyu ndi nkhuyu zoyamba kupsa; akaigwedeza zingokugwa m'kamwa mwa wakudya.