Nahum 3:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale mutero, moto udzakupserezanibe, ndipo lupanga lidzakukanthani, mudzapululuka ngati dzombe. Swanani ngati dzombe, chulukanani ngati ziwala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo moto udzatha iwe; lupanga lidzakuononga; lidzatha iwe ngati chirimamine; udzichulukitse ngati chirimamine, udzichulukitse ngati dzombe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumeneko moto udzakupserezani; lupanga lidzakukanthani ndipo lidzakuwonongani ngati likuwononga ziwala. Chulukanani ngati ziwala, chulukanani ngati dzombe!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo moto udzatha iwe; lupanga lidzakuononga; lidzatha iwe ngati cirimamine; udzicurukitse ngati cirimamine, udzicurukitse ngati dzombe.