Nahum 3:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nduna zanu zili ngati dzombe. Akuluakulu anu ali ngati ziwala, zimene zimangokangamira pa khoma kukazizira. Koma dzuŵa likamatuluka, zimauluka, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene amadziŵa kumene zapita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ovala korona ako akunga dzombe, ndi akazembe, ndi akazemba ako ngati ziwalamsatsi zakutera m'matchinga tsiku lachisanu, koma likafundukula dzuwa ziuluka nizithawa, ndi kumene zinakhalako sikudziwikanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akalonga ako ali ngati dzombe, akuluakulu ako ali ngati gulu la dzombe limene lamatirira pa khoma nthawi yozizira, koma pamene dzuwa latuluka limawuluka, ndipo palibe amene amadziwa komwe lapita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Obvala korona ako akunga dzombe, ndi akazembe, ndi akazembe ako ngati ziwalamsatsi zakutera m'macinga tsiku lacisanu, koma likafundukula dzuwa ziuluka nizithawa, ndi kumene zinakhalako sikudziwikanso.