Nahum 3:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe mfumu ya Aasiriya, nduna zako zaferatu. Akuluakulu ako apitiratu. Anthu ako amwazikira ku mapiri, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe woŵasonkhanitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Abusa ako aodzera, mfumu ya ku Asiriya; omveka ako apumula; anthu ako amwazika pamapiri, ndipo palibe wakuwasonkhanitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe mfumu ya ku Asiriya, abusa ako agona tulo; anthu ako olemekezeka amwalira. Anthu ako amwazikira ku mapiri popanda ndi mmodzi yemwe wowasonkhanitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Abusa ako aodzera, mfumu ya ku Asuri; omveka ako apumula; anthu ako amwazika pamapiri, ndipo palibe wakuwasonkhanitsa.