Nahum 3:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palibe mankhwala a bala lako, chilonda chako sichingapole. Onse amene amamva za iwe, amaomba m'manja mokondwa. Kodi alipo wina amene sadazilaŵepo nkhanza zako zosathazi?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Palibe chakulunzitsa kuthyoka kwako; bala lako liwawa; onse akumva mbiri yako akuombera manja; pakuti ndaniyo kuipa kwako sikunampitapitabe?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palibe chimene chingachize bala lako; chilonda chako sichingapole. Aliyense amene amamva za iwe amawomba mʼmanja chifukwa cha kugwa kwako, kodi alipo amene sanazilawepo nkhanza zako zosatha?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Palibe cakulunzitsa kutyoka kwako; bala lako liwawa; onse akumva mbiri yako akuombera manja; pakuti ndaniyo kuipa kwako sikunampitapitabe?