Nahum 3:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zonsezo zachitika chifukwa cha zonyansa zochuluka za Ninive, mkazi wachiwerewere uja. Ankakopa anthu ndi kukongola kwake konyenga. Ankanyengadi anthu a mitundu yonse ndi zadama zake nakopa mafuko ndi zithumwa zake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa cha chiwerewere chochuluka cha wachiwerewere wokongola, ndiye mkaziyo mwini nyanga, wakugulitsa amitundu mwa chiwerewere chake, ndi mabanja mwa nyanga zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zonsezi ndi chifukwa cha zilakolako za mkazi wachiwerewere, wokopa anthu uja, mkazi wochita zamatsenga, amene anakopa mitundu ya anthu ndi zachiwerewere zake, ndiponso anthu a mitundu ina ndi zaufiti zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa ca ciwerewere cocuruka ca waciwerewere wokongola, ndiye mkaziyo mwini nyanga, wakugulitsa amitundu mwa ciwerewere cace, ndi mabanja mwa nyanga zace.