Nahum 3:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ine sindikugwirizana nawe, ndidzakuvula ndi kukunyazitsa. Anthu a mitundu yonse adzaona maliseche ako, udzachita manyazi pamaso pa maiko onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndidzaphimba nkhope yako ndi nsalu yako yoyesa mthendene; ndipo ndidzaonetsa amitundu umaliseche wako, ndi mafumu manyazi ako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndikutsutsana nawe. Ndidzakuvula chovala chako. Anthu a mitundu ina ndidzawaonetsa umaliseche wako ndipo udzachita manyazi pamaso pa maufumu onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndidzaphimba nkhope yako ndi nsaru yako yoyesa mthendene; ndipo ndidzaonetsa amitundu umarisece wako, ndi maufumu manyazi ako.