Nehemiah 1:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adandiyankha kuti, “Anthu amene aja ali pa mavuto ndiponso ali ndi manyazi aakulu. Makoma a Yerusalemu ngogamukagamuka, ndipo zipata zake zidaonongeka ndi moto.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanena nane iwo, Otsalawo otsala andende uko kudzikoko akulukutika kwakukulu, nanyozedwa; ndi linga la Yerusalemu lapasuka, ndi zipata zake zatenthedwa ndi moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anandiyankha kuti, “Amene sanatengedwe ukapolo aja ali pa mavuto aakulu ndipo ali ndi manyazi. Khoma la Yerusalemu ndilogamukagamuka ndipo zipata zake zinatenthedwa ndi moto.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanena nane iwo, Otsalawo otsala andende uko ku dzikoko akulukutika kwakukuru, nanyozedwa; ndi linga la Yerusalemu lapasuka, ndi zipata zace zatenthedwa ndi moto.