Nehemiah 1:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidati, “Inu Chauta, Mulungu wakumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, mumasunga chipangano. Mumaonetsa chikondi chosasinthika kwa anthu amene amakukondani ndi kutsata malamulo anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinkati: “Inu Yehova, Mulungu wakumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa. Mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa onse amene amakukondani ndi kumvera malamulo anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkuru ndi woopsa, wakusunga pangano ndi cifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ace;