Nehemiah 1:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mukabwerera kwa Ine, mukamvera malamulo anga ndi kuŵatsatadi, ndiye kuti ngakhale anthu anu omwazikawo akhale kutali chotani, ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku mbali zonse ndi kubwera nawo ku malo amene ndidasankha kuti azidzandipembedza kumeneko.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma mukabwerera kudza kwa Ine, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita, angakhale otayika anu anali ku malekezero a thambo, ndidzawasonkhanitsa kuchokera komweko, ndi kubwera nao kumalo ndinawasankha kukhalitsako dzina langa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mukabwerera kwa Ine, mukamvera malamulo anga ndi kuwatsatadi, ndiye kuti ngakhale anthu anu atabalalika kutali chotani, Ine ndidzawasonkhanitsa kuchokera kumeneko ndi kubwera nawo ku malo amene ndinasankha kuti azidzayitanira dzina langa.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma mukabwerera kudza kwa Ine, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwacita, angakhale otayika anu anali ku malekezero a thambo, ndidzawasonkhanitsa kucokera komweko, ndi kubwera nao ku malo ndinawasankha kukhalitsako dzina langa.