Nehemiah 10:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ife otsalafe, ansembe, Alevi, alonda a pa Nyumba ya Mulungu, oimba nyimbo, atumiki a ku Nyumba ya Mulungu, ndi onse amene ankadzipatula kwa mitundu ina ya anthu ya m'maiko achilendo, kuti atsate Malamulo a Mulungu, tonse, pamodzi ndi akazi athu, ana athu ndi onse amene ali ndi nzeru zokwanira,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi anthu otsala, ansembe, Alevi, odikira, oimbira, Anetini, ndi onse anadzisiyanitsawo pa mitundu ya anthu a m'dziko kutsata chilamulo cha Mulungu, akazi ao, ana ao aamuna ndi aakazi, yense wodziwa ndi wozindikira,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ife otsalafe, ndiye kuti ansembe, Alevi, alonda a ku Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu, onse amene anadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina kuti atsate malamulo a Yehova, pamodzi ndi akazi athu, ana athu ndi onse amene ali ndi nzeru,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi anthu otsala, ansembe, Alevi, odikira, oyimbira, Anetini, ndi onse anadzisiyanitsawo pa mitundu ya anthu a m'dziko kutsata cilamulo ca Mulugu, akazi ao, ana ao amuna ndi akazi, yense wodziwa ndi wozindikira,