Nehemiah 10:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
tikuphatikana ndi abale athu olemekezeka, ndipo tikulonjeza molumbira kuti tidzayenda motsata Malamulo a Mulungu amene adaŵapereka Mose mtumiki wa Mulungu. Tidzamvera ndi kuchitadi zimene Malamulo a Chauta, Mulungu wathu, amanena. Tidzamveranso malangizo ndi miyambo yake yolamulidwa. Ndipo titembereredwe tikalephera kuchita zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amenewa anaumirira abale ao, omveka ao, nalowa m'temberero ndi lumbiro, kuti adzayenda m'chilamulo cha Mulungu anachipereka Mose mtumiki wa Mulungu, ndi kuti adzasunga ndi kuchita zonse atilamulira Yehova Ambuye wathu, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
tikuphatikana ndi abale athu wolemekezeka, ndipo tikulonjeza molumbira kuti tidzayenda motsata malamulo a Mulungu amene anapereka kudzera mwa Mose mtumiki wa Mulungu. Tilonjeza kumvera ndi kutsata bwino mawu onse, miyambo yonse ndi malangizo onse a Yehova. Yehova atilange ngati sitidzachita zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amenewa anaumirira abale ao, omveka ao, nalowa m'temberero ndi lumbiro, kuti adzayenda m'cilamulo ca Mulungu anacipereka Mose mtumiki wa Mulungu, ndi kuti adzasunga ndi kucita zonse atilamulira Yehova Ambuye wathu, ndi maweruzo ace, ndi malemba ace;