Nehemiah 10:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ngati anthu a mitundu ina ya m'dzikomo abwera ndi zinthu zamalonda kapena tirigu, kudzagulitsa pa tsiku la sabata, sitidzaŵagula pa tsiku limenelo, kapenanso pa tsiku loyera lina lililonse. Pa chaka chilichonse chachisanu ndi chiŵiri, tidzagoneka munda osaulima, ndipo tidzafafaniza ngongole zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo mitundu ya anthu a m'dziko akabwera nao malonda, ngakhale tirigu, tsiku la Sabata, kutsata malonda, sitidzagulana nao tsiku la Sabata, kapena dzuwa lina lopatulika, ndi kuti tidzaleka chaka chachisanu ndi chiwiri ndi mangawa ali onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngati anthu a mitundu ina abwera ndi zinthu za malonda, monga tirigu, kudzagulitsa pa tsiku la Sabata, sitidzawagula pa tsiku la Sabata kapena pa tsiku lina lililonse loyera. Pa chaka chilichonse cha chisanu ndi chiwiri tidzagoneka munda wosawulima ndipo tidzafafaniza ngongole zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo mitundu ya anthu a m'dziko akabwera nao malonda, ngakhale tirigu, dzuwa la Sabata, kutsata malonda, sitidzagulana nao dzuwa la Sabata, kapena dzuwa lina lopatulika, ndi kuti tidzaleka caka cacisanu ndi ciwiri ndi mangawa ali onse.