Nehemiah 10:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tiziperekanso ndalama zolipirira buledi woperekedwa, chopereka cha chakudya ndiponso nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku, zopereka za pa masabata, za pokhala mwezi, za pa masiku achikondwerero osankhidwa, zoperekera zinthu zopatulika ndiponso nsembe zopepesera machimo a Aisraele, kudzanso zoperekera china chilichonse chofunika pa ntchito ya ku Nyumba ya Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kulipereka mkate woonekera, ndi nsembe yaufa yosaleka, ndi nsembe yopsereza yosaleka, ya masabata, ya pokhala miyezi, kuliperekera nyengo zoikika ndi zopatulikira, ndi nsembe za zolakwa za kutetezera Israele zoipa, ndi ntchito zonse za nyumba ya Mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndalamayi izithandiza kulipirira buledi wa pa tebulo, chopereka cha chakudya cha nthawi zonse, zopereka zopsereza za nthawi zonse, zopereka za pa tsiku la Sabata, za pachikondwerero cha Mwezi Watsopano, za pa masiku a chikondwerero osankhika, zopereka za zinthu zopatulika, zopereka za nsembe yopepesera machimo a Aisraeli ndi ntchito ina iliyonse ya ku Nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuliperekera mkate woonekera, ndi nsembe yaufa yosaleka, ndi nsembe yopsereza yosaleka, ya masabata, ya pokhala miyezi, kuliperekera nyengo zoikika ndi zopatulikira, ndi nsembe za zolakwa za kutetezera Israyeli zoipa, ndi nchito zonse za nyumba ya Mulungu wathu.