Nehemiah 10:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ife ansembe, Alevi ndi anthu wamba tidzachita maele, kuti tisankhe mabanja amene adzapereke nkhuni ndi kubwera nazo ku Nyumba ya Mulungu wathu, pa nthaŵi zake zoikidwa, chaka ndi chaka, kuti azipserezera nsembe za pa guwa la Chauta, Mulungu wathu, monga mudalembedwera m'Malamulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tinalota maere, ansembe, Alevi, ndi anthu, a chopereka cha nkhuni, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu, monga mwa nyumba za makolo athu, pa nyengo zoikika chaka ndi chaka, kuzisonkha pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu, monga mulembedwa m'chilamulo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ife ansembe, Alevi ndi anthu onse, tachita maere kuti tidziwe pamene banja lathu lililonse lidzabweretsa ku nyumba ya Mulungu wathu pa nthawi yoyikika ya chaka zopereka za nkhuni zoyaka pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tinalota maere, ansembe, Alevi, ndi anthu, a copereka ca nkhuni, kubwera nazo ku nyumba ya Mulungu wathu, monga mwa nyumba za makolo athu, pa nyengo zoikika caka ndi caka, kuzisonkha pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu, monga mulembedwa m'cilamulo;