Nehemiah 10:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tidzaperekanso kwa Mulungu ana athu aamuna oyamba kubadwa. Ana a ng'ombe oyamba kubadwa ndiponso ana oyamba kubadwa a nkhosa ndi a mbuzi zathu, tidzapereka kwa ansembe amene amatumikira ku Nyumba ya Mulungu, monga mudalembedwera m'Malamulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m'chilamulo, ndi oyamba a ng'ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m'nyumba ya Mulungu wathu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tidzabweranso nawo ku Nyumba ya Mulungu, kwa ansembe amene amatumikira ku Nyumba ya Mulungu ana athu aamuna oyamba kubadwa ndi ana angʼombe oyamba kubadwa monga zalembedwera mu Malamulo. Tidzaperekanso ana oyamba kubadwa a ziweto zathu ndi ana ankhosa oyamba kubadwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m'cilamulo, ndi oyamba a ng'ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo ku nyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m'nyumba ya Mulungu wathu;