Nehemiah 10:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembe, mdzukulu wa Aroni, adzakhale pamodzi ndi Alevi, pamene Aleviwo akulandira zigawo zachikhumizo. Ndipo Alevi adzabwera ndi zigawozo ku Nyumba ya Mulungu wathu, ku zipinda zosungiramo katundu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe mwana wa Aroni azikhala ndi Alevi, polandira Alevi limodzilimodzi la magawo khumi; ndi Alevi azikwera nalo limodzi la magawo khumi mwa limodzilimodzi la magawo khumi kunyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda, kunyumba ya chuma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe, mdzukulu wa Aaroni azikhala pamodzi ndi Alevi pamene akulandira chakhumi. Ndipo Alevi azibwera ndi chakhumicho ku nyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda zosungiramo chuma.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe mwana wa Aroni azikhala ndi Alevi, polandira Alevi limodzi limodzi la magawo khumi; ndi Alevi azikwera nalo limodzi la magawo khumi mwa limodzi limodzi la magawo khumi ku nyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda, ku nyumba ya cuma.