Nehemiah 10:39 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele ndiponso a m'banja la Levi adzapereka tirigu, vinyo ndi mafuta kuzipinda kosungira ziŵiya za m'malo opatulika, ndiponso kokhala ansembe amene akutumikira, pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, ndi anthu oimba nyimbo. Ndithu ife tidzasamala Nyumba ya Mulungu wathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ana a Israele ndi ana a Levi, azibwera nayo nsembe yokweza yatirigu, ndi yavinyo ndi yamafuta, kuzipinda kuli zipangizo za malo opatulika, ndi ansembe akutumikira, ndi odikira, ndi oimbira; kuti tisasiye nyumba ya Mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Israeli, kuphatikiza zidzukulu za Alevi, azipititsa zopereka za tirigu, vinyo ndi mafuta ku zipinda zosungiramo katundu wopatulika, komanso kokhala ansembe amene akutumikira pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu ndi anthu oyimba nyimbo. “Kwambiri ife sitidzaleka kusamala Nyumba ya Mulungu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ana a Israyeli ndi ana a Levi, azibwera nayo nsembe yokweza yatirigu, ndi yavinyo ndi yamafuta, kuzipinda kuli zipangizo za malo opatulika, ndi ansembe akutumikira, ndi odikira, ndi oyimbira; kuti tisasiye nyumba ya Mulungu wathu.