Nehemiah 11:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo atsogoleri a mabanja a Aisraele ankakhala ku Yerusalemu. Tsono anthu ena onse adachita maele kuti apeze munthu mmodzi pa anthu khumi aliwonse oti azikhala ku Yerusalemu, mzinda wopatulikawo, ndipo anthu asanu ndi anai otsala azikhalabe m'midzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akulu a anthu anakhala m'Yerusalemu; anthu otsala omwe anachita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale m'Yerusalemu, mudzi wopatulika, ndi asanu ndi anai akhumi m'midzi ina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyo atsogoleri a anthu ankakhala ku Yerusalemu. Tsono anthu ena onse anachita maere kuti apeze munthu mmodzi pa anthu khumi aliwonse kuti azikhala ku Yerusalemu, mzinda wopatulika. Anthu asanu ndi anayi otsalawo ankakhala mʼmidzi yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akuru anthu anakhala m'Yerusalemu; anthu otsala omwe anacita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale m'Yerusalemu, mudzi wopatulika, ndi asanu ndi anai a khumi m'midzi yina.