Nehemiah 11:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndiponso achibale ao amene anali ankhondo olimba mtima. Onse pamodzi analipo 128, ndipo kapitao wao anali Zabidiele, mwana wa Hagedolimu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi abale ao, ngwazi zamphamvu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu; ndi woyang'anira wao ndiye Zabidiele mwana wa Hagedolimu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndi abale ake. Onse pamodzi anali 128 ndipo anali anthu olimba mtima kwambiri. Mtsogoleri wawo wamkulu anali Zabidieli mwana wa Hagedolimu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi abale ao, ngwazi zamphamvu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu; ndi woyang'anira wao ndiye Zabidiyeli mwana wa Hagedolimu.