Nehemiah 11:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthu otumikira ku Nyumba ya Mulungu ankakhala ku Ofele, mu Yerusalemu, ndipo Ziha ndi Gisipa ankaŵayang'anira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Anetini anakhala m'Ofele, ndi Ziha, ndi Gisipa anali oyang'anira Anetini.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma antchito a ku Nyumba ya Mulungu ankakhala pa phiri la Ofeli, ndipo Ziha ndi Gisipa ndiwo anali kuwayangʼanira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Anetini anakhala m'Ofeli, ndi Ziya, ndi Gisipa anali oyang'anira Anetini.