Nehemiah 11:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kapitao wa Alevi ku Yerusalemu anali Uzi, mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika. Anali mmodzi mwa zidzukulu za a Asafu, amene anali oimba nyimbo zofunika pa miyambo ya m'Nyumba ya Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo woyang'anira wa Alevi m'Yerusalemu ndiye Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika; mwa ana a Asafu oimbira ena anayang'anira ntchito ya m'nyumba ya Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wamkulu wa Alevi mu Yerusalemu anali Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika. Uzi anali mmodzi wa zidzukulu za Asafu, amene anali oyimba nyimbo pa nthawi zachipembedzo mʼNyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo woyang'anira wa Alevi m'Yerusalemu ndiye Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika; mwa ana a Asafu oyimbira ena anayang'anira nchito ya m'nyumba ya Mulungu.