Nehemiah 11:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele wamba ambiri, pamodzi ndi ansembe, Alevi, anthu otumikira ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso zidzukulu za atumiki a Solomoni, onsewo ankakhala m'midzi mwao, aliyense m'dera la choloŵa chake. Koma akuluakulu a m'chigawo cha Yuda anali atakhazikika ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Awa tsono ndi akulu a dziko okhala m'Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa cholowa chake m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, ndi Alevi, ndi Anetini, ndi ana a akapolo a Solomoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli wamba, ansembe, Alevi, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ndiponso zidzukulu za antchito a Solomoni ankakhala mʼmidzi yawo, aliyense mu dera lake. Koma atsogoleri a chigawo cha Yuda anali atakhazikika mu Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Awa tsono ndi akulu a dziko okhala m'Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa colowa cace m'midzi mwao, ndiwo Israyeli, ansembe, ndi Alevi, ndi Anetini, ndi ana a akapolo a Solomo.