Nehemiah 12:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi ya Eliyasibu, Yoyada, Yohanani ndi Yaduwa, amene anali akulu a ansembe, padalembedwa maina a atsogoleri a mabanja a Alevi ndi a ansembe, mpaka pa nthaŵi imene mfumu Dariusi wa ku Persiya ankalamulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'masiku a Eliyasibu, Yoyada, Yohanani, ndi Yaduwa, Alevi analembedwa akulu a nyumba za makolo; ansembe omwe, mpaka ufumu wa Dariusi wa ku Persiya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi ya Eliyasibu, Yoyada, Yohanani ndi Yaduwa panalembedwa atsogolera a mabanja a Alevi ndi a ansembe mpaka pa nthawi ya ulamuliro wa Dariyo Mperisi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'masiku a Ehasibi, Yoyada, Yohanana, ndi Yoduwa, Alevi analembedwa akuru a nyumba za makolo; ansembe omwe, mpaka ufumu wa Dariyo wa ku Perisiya.