Nehemiah 12:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atsogoleri a Alevi, Hasabiya, Serebiya ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyele, ankathandizana ndi abale ao poimba nyimbo zotamanda ndi zothokoza, monga momwe Davide, munthu wa Mulungu, adaaŵalamulira kuti gulu liziimba molandizana ndi gulu linzake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi akulu a Alevi: Hasabiya, Serebiya, ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyele, ndi abale ao openyana nao, kulemekeza ndi kuyamika, monga mwa lamulo la Davide munthu wa Mulungu, alonda kupenyana alonda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo atsogoleri a Alevi awa, Hasabiya, Serebiya, Yesuwa mwana wa Kadimieli ndi abale awo, ankayimba nyimbo zotamanda ndi zothokoza molandizana. Gulu limodzi linkavomerezana ndi linzake monga mmene Davide munthu wa Mulungu analamulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi akuru a Alevi: Hasabiya, Serebiya, ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyeli, ndi abale ao openyana nao, kulemekeza ndi kuyamika, monga mwa lamulo la Davide munthu wa Mulungu, alonda kupenyana alonda.