Nehemiah 12:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene anthu adati apereke kwa Mulungu khoma lozinga mzinda wa Yerusalemu, adaitana Alevi kuchokera konse kumene ankakhala, kuti abwere ku Yerusalemu kudzachita mwambo wopereka khomalo mokondwera, mothokoza ndiponso poimba pamodzi ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi mapangwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo popereka linga la Yerusalemu anafunafuna Alevi m'malo mwao monse, kubwera nao ku Yerusalemu, kuti achite kuperekaku mokondwera, ndi mayamiko, ndi kuimbira, ndi nsanje, zisakasa, ndi azeze.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa mwambo wopereka khoma la Yerusalemu anayitana Alevi kulikonse kumene ankakhala kuti abwere ku Yerusalemu ku mwambo wopereka khoma kwa Mulungu, mwachimwemwe ndi mothokoza poyimba nyimbo pamodzi ndi ziwiya za malipenga, azeze ndi apangwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo popereka linga la Yerusalemu anafunafuna Alevi m'malo mwao monse, kubwera nao ku Yerusalemu, kuti acite kuperekaku mokondwera, ndi mayamiko, ndi kuyimbira, ndi nsanje, zisakasa, ndi azeze.