Nehemiah 12:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ineyo ndidadza nawo akuluakulu a ku dziko la Yuda ndipo ndidakwera nawo pa khoma. Ndidasankha magulu aŵiri mwa iwo, kuti aziyenda mu mdipiti ndi kumathokoza Mulungu. Mdipiti wina unkadzera cha ku dzanja lamanja pa khoma mpaka kukafika ku Chipata cha Kudzala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndinakwera nao akulu a Yuda pa lingali, ndinaikanso oyamikira magulu awiri akulu oyenda molongosoka; lina loyenda ku dzanja lamanja palinga kunka ku Chipata cha Kudzala;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinabwera nawo atsogoleri a dziko la Yuda ndi kukwera nawo pa khoma. Ndipo ndinasankha magulu awiri akuluakulu oyimba nyimbo za matamando. Gulu limodzi linadzera mbali ya ku dzanja lamanja pa khoma mpaka ku Chipata cha Kudzala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndinakwera nao akuru a Yuda pa lingali, ndinaikanso oyamikira magulu awiri akuru oyenda molongosoka; lina loyenda ku dzanja lamanja palinga kumka ku cipata ca kudzala;