Nehemiah 12:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuchokera ku Chipata cha Kasupe, adakwera pa makwerero opita ku mzinda wa Davide, pa njira yotsatira khoma, chakumtunda kwa nyumba ya Davide, mpaka kukafika ku Chipata cha Madzi, kuvuma kwa mzinda wa Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi ku Chipata cha ku Chitsime, ndi kundunji kwao, anakwerera pa makwerero a mudzi wa Davide, potundumuka linga, popitirira pa nyumba ya Davide, mpaka ku Chipata cha Madzi kum'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera ku Chipata cha Kasupe anayenda nakakwera makwerero opita ku mzinda wa Davide pa njira yotsatira khoma, chakumtundu kwa nyumba ya Davide mpaka ku Chipata cha Madzi, mbali ya kummawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi ku cipata ca kucitsime, ndi kundunji kwao, anakwerera pa makwerero a mudzi wa Davide, potundumuka linga, popitirira pa nyumba ya Davide, mpaka ku cipata ca kumadzi kum'mawa.