Nehemiah 12:38 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mdipiti wina wa anthu othokoza Mulungu udadzera chakumanzere kwa khomalo, ndipo ine ndidautsata pambuyo, poyenda pa khoma pamodzi ndi theka lina la akuluakulu. Tidapitirira Nsanja ya Ng'anjo, kukafika ku Khoma Lotambasuka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi gulu lina la oyamikira linamuka mokomana nao, ndi ine ndinawatsata, pamodzi ndi limodzi la magawo awiri la anthu palinga, napitirira pa Nsanja ya Ng'anjo, mpaka kulinga lachitando;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gulu loyimba lachiwiri linadzera mbali ya kumanzere kwa khomalo. Tsono ine ndi theka lina la atsogoleri aja tinkalitsata pambuyo tikuyenda pamwamba pa khomalo. Tinapitirira Nsanja ya Ngʼanjo mpaka ku Khoma Lotambasuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi gulu lina la oyamikira linamuka mokomana nao, ndi ine ndinawatsata, pamodzi ndi limodzi la magawo awiri la anthu palinga, napitirira pa nsanja ya ng'anjo, mpaka ku linga lacitando;