Nehemiah 12:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tidadzeranso pa Chipata cha Efuremu, pa Chipata Chakale, pa Chipata cha Nsomba, pa Nsanja ya Hananele, pa Nsanja ya Zana, mpaka kukafika ku Chipata cha Nkhosa. Ndipo potsiriza tidakaima ku Chipata cha Mlonda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi pamwamba pa Chipata cha Efuremu, ndi ku Chipata Chakale, ndi ku Chipata Chansomba, ndi Nsanja ya Hananele, ndi Nsanja ya Zana, mpaka kuchipata chankhosa; ndipo anaima ku Chipata cha Akaidi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tinadutsanso Chipata cha Efereimu, Chipata cha Yesana, Chipata cha Nsomba, Nsanja ya Hananeli, Nsanja ya Zana mpaka kukafika ku Chipata cha Nkhosa. Ndipo mdipiti uwu unakayima pa Chipata cha Mlonda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi pamwamba pa cipata ca Efraimu, ndi ku cipata cakale, ndi ku cipata cansomba, ndi nsanja ya Hananeli, ndi nsanja ya Hameya, mpaka ku cipata cankhosa; ndipo anaima ku cipata cakaidi.