Nehemiah 12:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku limenelo anthu adapereka nsembe zochuluka, ndipo adakondwa kwakukulu, popeza kuti Mulungu ndiye adaŵakondwetsa. Akazi nawonso, pamodzi ndi ana, adakondwa, ndipo kukondwa kwa anthu a ku Yerusalemu kudamveka patali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaphera nsembe zambiri tsiku lija, nasekerera; pakuti Mulungu anawakondweretsa ndi chimwemwe chachikulu; ndi akazi omwe ndi ana anakondwera; ndi chikondwerero cha Yerusalemu chinamveka kutali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku limenelo anthu anapereka nsembe zambiri ndipo anakondwera chifukwa Mulungu anawapatsa chimwemwe chachikulu. Nawonso akazi ndi ana anakondwera ndipo kukondwa kwa anthu a mu mzinda wa Yerusalemu kunamveka kutali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaphera nsembe zambiri tsiku lija, nasekerera; pakuti Mulungu anawakondweretsa ndi cimwemwe cacikuru; ndi akazi omwe ndi ana anakondwera; ndi cikondwerero ca Yerusalemu cinamveka kutali.