Nehemiah 12:44 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo padasankhidwa anthu oyang'anira zipinda zosungiramo zopereka zaufulu, zipatso zoyamba kucha, ndi zopereka zachikhumi. Anthuwo ankasonkhanitsa zopereka potsata Malamulo a Mose, kuti azipereka kwa ansembe ndi Alevi, kuchokera ku minda ya midzi yonse. Pakuti Ayuda ankakondwera nawo ansembe ndi Alevi otumikirawo,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku lomwelo anaika anthu asunge zipinda za chuma, za nsembe zokweza, za zipatso zoyamba, ndi za limodzilimodzi la magawo khumi, kulonga m'mwemo, monga mwa minda ya midzi, magawo onenedwa ndi chilamulo, akhale a ansembe ndi Alevi; popeza Yuda anakondwera nao ansembe ndi Alevi akuimirirako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo panasankhidwa anthu oyangʼanira zipinda zosungiramo zopereka zaufulu, zipatso zoyamba kucha, zopereka za chakhumi. Anthuwo ankasonkhanitsa zopereka kuchokera ku minda ya midzi yonse kuti azipereke kwa ansembe ndi Alevi malingana ndi malamulo. Izi zinali chomwechi chifukwa Ayuda ankakondwera ndi utumiki wa ansembe ndi Alevi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku lomwelo anaika anthu asunge zipinda za cuma, za nsembe zokweza, za zipatso zoyamba, ndi za limodzi limodzi la magawo khumi, kulonga m'mwemo, monga mwa minda ya midzi, magawo onenedwa ndi cilamulo, akhale a ansembe ndi Alevi; popeza Yuda anakondwera nao ansembe ndi Alevi lakuimirirako.