Nehemiah 12:45 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
chifukwa ankachita zimene Mulungu wao adaalamula, makamaka mwambo wopatulira zinthu. Oimba nyimbo ndiponso alonda a ku Nyumba ya Mulungu nawonso ankagwira ntchito zao potsata lamulo la Davide ndi Solomoni mwana wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo anasunga udikiro wa Mulungu wao, ndi udikiro wa mayeretsedwe; momwemonso oimbira ndi odikira, monga mwa lamulo la Davide ndi la Solomoni mwana wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwowa ankagwira ntchito ya Mulungu wawo, makamaka mwambo woyeretsa zinthu. Nawonso oyimba nyimbo ndi olonda ku Nyumba ya Mulungu anagwira ntchito zawo monga Davide ndi mwana wake Solomoni analamula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo anasunga udikiro wa Mulungu wao, ndi udikiro wa mayeretsedwe; momwemonso oyimbira ndi odikira, monga mwa lamulo la Davide ndi la Solomo mwana wace.