Nehemiah 12:47 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi ya Zerubabele ndi Nehemiya, anthu a m'dziko lonse la Israele ankapereka tsiku ndi tsiku mphatso zofunika kwa anthu oimba nyimbo ndiponso kwa alonda a ku Nyumba ya Mulungu. Ankaikanso padera chigawo cha Alevi, ndipo Aleviwo nawonso ankaika padera chigawo cha ansembe, adzukulu a Aroni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi Aisraele onse m'masiku a Zerubabele, ndi m'masiku a Nehemiya, anapereka magawo a oimbira ndi odikira, monga mudafunika tsiku ndi tsiku; nawapatulira Alevi; ndi Alevi anawapatulira ana a Aroni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mu nthawi ya Zerubabeli ndi Nehemiya, Aisraeli onse anakapereka mphatso tsiku ndi tsiku kwa anthu oyimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu. Ankayikanso padera chigawo cha zopereka cha Alevi. Nawonso Alevi ankayika padera chigawo cha zopereka cha ansembe, zidzukulu za Aaroni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi Aisrayeli onse m'masiku a Zerubabele, ndi m'masiku a Nehemiya, anapereka magawo a oyimbira ndi odikira, monga mudafunika tsiku ndi tsiku; nawapatulira Alevi; ndi Alevi anawapatulira ana a Aroni.