Nehemiah 13:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku limenelo adaŵerenga buku la Mose, anthu onse alikumva. Ndipo adafika pa mau akuti, “Mwamoni kapena Mmowabu asaloŵe konse mu msonkhano wa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku lomwelo anawerenga m'buku la Mose m'makutu a anthu, napeza m'menemo kuti Aamoni ndi Amowabu asalowe mu msonkhano wa Mulungu kunthawi yonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku limenelo anawerenga buku la Mose anthu akumva. Ndipo anapeza mawu akuti, Mwamoni kapena Mmowabu asalowe konse mu msonkhano wa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku lomwelo anawerenga m'buku la Mose m'makutu a anthu, napeza m'menemo kuti Aamoni ndi Amoabu asalowe mu msonkhano wa Mulungu ku nthawi yonse;