Nehemiah 13:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidapezanso kuti Alevi sankaŵapatsa magawo ao amene ankayenera kulandira. Choncho Aleviwo, pamodzi ndi anthu oimba nyimbo amene ankagwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu, adathaŵa, aliyense kupita ku munda wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinazindikiranso kuti sanapereke kwa Alevi magawo ao; m'mwemo Alevi ndi oimbira adathawira yense kumunda wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinapezanso kuti Alevi sankalandira magawo awo amene amayera kulandira. Chotsatira chake Alevi onse pamodzi ndi oyimba nyimbo amene ankagwira ku Nyumba ya Mulungu anathawa, aliyense kupita ku munda wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinazindikiranso kuti sanapereka kwa Alevi magawo ao; m'mwemo Alevi ndi oyimbira adathawira yense ku munda wace.