Nehemiah 13:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho ndidaŵadzudzula akuluakulu aja kuti, “Kodi chifukwa chiyani Nyumba ya Mulungu yasiyidwa chonchi?” Ndipo ndidasonkhanitsa anthu aja ndi kuŵaikanso pa ntchito zimene ankazigwira
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero ndinatsutsana nao olamulira, ndinati, Yasiyidwiranji nyumba ya Mulungu? Ndipo ndinawasonkhanitsa, ndi kuwaika m'malo mwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ndinadzudzula akuluakulu aja ndipo ndinawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani Nyumba ya Mulungu yasiyidwa?” Ndipo ine ndinawayitanitsa pamodzi ndi kuwayika mʼmalo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero ndinatsutsana nao olamulira, ndinati, Yasiyidwiranji nyumba ya Mulungu? Ndipo ndinawasonkhanitsa, ndi kuwafka m'malo mwao.