Nehemiah 13:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Mulungu wanga, mundikumbukire ine pa zimenezi. Musaiŵale ntchito zanga zabwino zimene ndachitira Nyumba ya Mulungu wanga pofuna kumtumikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mundikumbukire Mulungu wanga mwa ichi, nimusafafanize zokoma zanga ndinazichitira nyumba ya Mulungu wanga, ndi maudikiro ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Mulungu wanga, mundikumbukire pa zimenezi, ndipo musafafanize ntchito zanga zimene ndachita mokhulupirika pa Nyumba yanu pofuna kukutumikirani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mundikumbukile Mulungu wanga mwa ici, nimusafafanize zokoma zanga ndinazicitira nyumba ya Mulungu wanga, ndi maudikiro ace.