Nehemiah 13:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo ndidaona anthu m'dziko la Yuda akuponda ndi kufinya mphesa pa tsiku la sabata. Ena ankaunjika tirigu milumilu, nkumasenzetsa abulu. Enanso ankatenga vinyo, mphesa, nkhuyu, ndiponso katundu wa mtundu uliwonse, nkumabwera naye ku Yerusalemu, pa tsiku la sabata. Tsono ndidaŵachenjeza kuti asamagulitse chakudya pa tsiku la sabata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku awa ndinaona ku Yuda ena akuponda mphesa m'choponderamo tsiku la Sabata, ndi akubwera nayo mitolo ya tirigu, ndi kuisenzetsa pa abulu; momwemonso vinyo, mphesa, ndi nkhuyu, ndi zosenza zilizonse, zimene analowa nazo m'Yerusalemu tsiku la Sabata, ndipo ndinawachitira umboni wakuwatsutsa tsikuli anagulitsa zakudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyo ndinaona anthu a mu Yuda akuponda ndi kufinya mphesa pa tsiku la Sabata. Ena ankawunjika tirigu milumilu ndi kumasenzetsa abulu. Enanso ankabwera ndi vinyo, mphesa, mkuyu ndi katundu wa mitundumitundu ku Yerusalemu pa tsiku la Sabata. Choncho ndinawachenjeza za kugulitsa zakudya pa tsiku la Sabata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku awa ndinaona ku Yuda ena akuponda mphesa m'coponderamo dzuwa la Sabata, ndi akubwera nayo mitolo ya tirigu, ndi kuisenzetsa pa aburu; momwemonso vinyo, mphesa, ndi nkhuyu, ndi zosenza ziri zonse, zimene analowa nazo m'Yerusalemu dzuwa la Sabata, ndipo ndinawacitira umboni wakuwatsutsa tsikuti anagulitsa zakudya.