Nehemiah 13:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nawonso anthu ena a ku Tiro okhala mu Yerusalemu, ankabwera ndi nsomba ndi zamalonda za mtundu uliwonse, nkumazigulitsa pa tsiku la sabata kwa anthu a m'dziko la Yuda ndiponso kwa anthu okhala mu mzinda wa Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anakhalanso m'menemo a ku Tiro, obwera nazo nsomba, ndi malonda ali onse, nagulitsa tsiku la Sabata kwa ana a Yuda ndi m'Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nawonso anthu a ku Turo amene ankakhala mu Yerusalemu ankabweretsa nsomba ndi akatundu ena onse amalonda kudzagulitsa pa Sabata kwa anthu a mʼdziko la Yuda ndi a mu Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anakhalanso m'menemo a ku Turo, obwera nazo nsomba, ndi malonda ali onse, nagulitsa dzuwa la Sabata kwa ana a Yuda ndi m'Yerusalemu.