Nehemiah 13:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo ndidadzudzula atsogoleri a Ayuda, ndipo ndidaŵafunsa kuti, “Monga simukuzindikira choipa chimene mukuchitachi pakuipitsa tsiku la sabata chonchi?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndinatsutsana nao aufulu a Yuda, ndinanena nao, Chinthu chanji choipa ichi muchichita, ndi kuipsa nacho tsiku la Sabata?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndinadzudzula anthu olemekezeka a dziko la Yuda. Ndinawafunsa kuti, “Nʼchoyipa chanji mukuchitachi, kumayipitsa tsiku la Sabata chotere?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndinatsutsana nao aufulu a Yuda, ndinanena nao, Cinthu canji coipa ici mucicita, ndi kuipsa naco dzuwa la Sabata?