Nehemiah 13:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake ndikulamula kuti pamene kuziyamba kuda, tsiku la sabata lisanayambike, azitseka zipata zonse za Yerusalemu, ndipo asazitsekule mpaka tsiku la sabata litapita. Ndidaika antchito anga ena oyang'anira pa zipata, kuti katundu aliyense asaloŵe mumzindamo pa tsiku la sabata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, kukadayamba chizirezire pa zipata za Yerusalemu, losafika Sabata, ndinawauza atseke pamakomo; ndinawauzanso kuti asatsegulepo, koma litapita Sabata ndipo; ndipo ndinaimika anyamata anga ena pazipata, kuti pasalowe katundu tsiku la Sabata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake ndikulamula kuti pamene kuyamba kuda, tsiku la Sabata lisanayambe, azitseka zipata zonse za Yerusalemu ndipo asazitsekule mpaka sabata litatha. Ndinayika ena mwa antchito anga oyangʼanira pa zipata kuti katundu aliyense asalowe mu Yerusalemu pa tsiku la Sabata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, kukadayamba cizirezire pa zipata za Yerusalemu, losafika Sabata, ndinawauza atseke pamakomo; ndinawauzanso kuti asatsegulepo, koma litapita Sabata ndipo; ndipo ndinaimika anyamata anga ena pazipata, kuti pasalowe katundu dzuwa la Sabata.