Nehemiah 13:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja ameneŵa sadapite kukakomana ndi ana a Aisraele, kuti akaŵapatse buledi ndi madzi. M'malo mwake adalemba Balamu kuti aŵatemberere. Komabe Mulungu wathu matembererowo adaŵasandutsa madalitso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza sanawachingamire ana a Israele ndi chakudya ndi madzi, koma anawalemberera Balamu awatemberere; koma Mulungu wathu anasanduliza tembererolo likhale mdalitso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paja iwowa sanawachingamire Aisraeli kukawapatsa chakudya ndi madzi. Mʼmalo mwake analemba ganyu Baalamu kuti adzawatemberere. Komabe Mulungu wathu anasandutsa tembererolo kukhala mdalitso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza sanawacingamira ana a Israyeli ndi cakudya ndi madzi, koma anawalemberera Balamu awatemberere; koma Mulungu wathu anasanduliza tembererolo likhale mdalitso.