Nehemiah 13:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ndidaŵachenjeza ndipo ndidaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukugona pafupi ndi khoma? Mukachitanso zimenezi ndidzakumangani.” Kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka m'tsogolo mwake, anthuwo sadabwerenso pa tsiku la sabata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndinawachitira umboni wakuwatsutsa, ndinanena nao, Mugoneranji pafupi pa linga? Mukateronso ndikuthirani manja. Kuyambira pomwepo sanafikenso pa Sabata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndinawachenjeza ndi kuwafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukugona pafupi ndi khoma? Ngati muchitanso zimenezi, ine ndidzakugwirani.” Kuyambira nthawi imeneyo, sanabwerenso pa tsiku la Sabata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndinawacima umboni wakuwatsutsa, ndinanena nao, Mugoneranji pafupi pa linga? mukateronso ndikuthirani manja. Kuyambira pomwepo sanafikanso pa Sabata.