Nehemiah 13:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka ndidaŵalamula Alevi kuti adziyeretse ndipo abwere kudzalonda pa zipata, kuti tsiku la sabata lisungike ngati lopatulika. Inu Mulungu wanga, mukumbukire zimenezinso pondikomera mtima, ndipo mundisunge potsata chikondi chanu chachikulu chosasinthika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula tsiku la Sabata. Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndinalamulira Alevi kuti adziyeretse okha ndi kubwera kudzalonda pa zipata ndi cholinga choti tsiku la Sabata likhale tsiku loyera. Inu Mulungu wanga, kumbukireninso ine pa zimenezi ndipo mundisunge malingana ndi chikondi chanu chachikulu chosasinthika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula dzuwa la Sabata. Mundikumbukire Icinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa cifundo canu cacikuru.