Nehemiah 13:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndidakangana nawo ndi kuŵatemberera. Ndidamenya ena mwa iwo ndi kuŵazula tsitsi. Ndipo ndidaŵalumbiritsa m'dzina la Mulungu kuti, “Musadzakwatitse ana anu aakazi kwa amuna achilendo, ndipo ana anu aamuna ndi inu nomwe musakwatire akazi achilendo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinatsutsana nao, ndi kuwatemberera, ndi kukantha ena a iwo, ndi kumwetula tsitsi lao, ndi kuwalumbiritsa pa Mulungu ndi kuti, Musapereka ana anu akazi kwa ana ao amuna, kapena kutengera ana anu amuna, kapena a inu nokha, ana ao akazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ndinakangana nawo ndi kuwatemberera. Ndinamenya ena mwa anthuwo ndi kuzula tsitsi lawo. Ine ndinawalumbiritsa mʼdzina la Mulungu kuti, “Inu musapereke ana anu aakazi kuti akwatiwe ndi ana awo aamuna kapena inuyo ngakhale ana anu aamuna kukwatira ana awo aakazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika