Nehemiah 13:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi Solomoni mfumu ya Aisraele suja adachimwa chifukwa cha akazi otereŵa? Pakati pa mitundu ya pansi pano panalibe mfumu yofanafana naye. Mulungu ankamkonda ndipo adamuika kuti akhale mfumu ya Aisraele onse. Komabe akazi achilendo adachimwitsa ngakhale iyeyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanga Solomoni mfumu ya Israele sanachimwe nazo zinthu izi? Chinkana mwa amitundu ambiri panalibe mfumu ngati iye, ndi Mulungu wake anamkonda, ndi Mulungu wake anamlonga mfumu ya Aisraele onse; koma ngakhale iye, akazi achilendo anamchimwitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi Solomoni mfumu ya Israeli suja anachimwa chifukwa cha ukwati ngati umenewu. Pakati pa mitundu yambiri panalibe mfumu ngati iyi. Iye anakondedwa ndi Mulungu wake, ndipo Mulungu anamuyika kukhala mfumu ya Israeli yense, koma iyeyo anachimwa chifukwa cha akazi achilendo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanga Solomo mfumu ya Israyeli sanacimwa nazo zinthu izi? cinkana mwa amitundu ambiri panalibe mfumu ngati iye, ndi Mulungu wace anamkonda, ndi Mulungu wace anamlonga mfumu ya Aisrayeli onse; koma ngakhale iye, akazi acilendo anamcimwitsa.