Nehemiah 13:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mmodzi mwa ana aamuna a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe uja, anali atakwatira mwana wa Sanibalati wa ku Horoni. Nchifukwa chake ndidampirikitsa kuti achoke ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma wina wa ana a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe, anali mkamwini wa Sanibalati Muhoroni; chifukwa chake ndinampirikitsa kumchotsa kwa ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmodzi mwa ana aamuna a Yehoyada mwana Eliyasibu mkulu wa ansembe nʼkuti nthawi imeneyi ali mpongozi wa Sanibalati wa ku Horoni. Choncho ndinamuthamangitsa pamaso panga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma wina wa ana a Yoyada, mwana wa Eliasibu mkuru wa ansembe, anali mkamwini wa Sanibalati Mhoroni; cifukwa cace ndinampitikitsa kumcotsa kwa ine.